2 Samuel 5:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo ukakonzeke, chifukwa ndiye kuti Chauta wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukayende mofulumira, chifukwa izi zikasonyeza kuti Yehova ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova waturuka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.