2 Samuel 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Davide ndi anthu ake adapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi. Ayebusiwo anali nzika za dzikolo. Anthuwo adauza Davide kuti, “Sudzaloŵa muno ai. Anthu akhungu ndi anthu opunduka ndiwo adzakupirikitse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ndi anthu ace anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ajebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupitikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno.