2 Samuel 5:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tsiku limenelo Davide adati, “Aliyense wofuna kuti akakanthe Ayebusi, ayenera kudzera m'ngalande ya madzi, kuti akaphe opunduka ndi akhunguwo amene mtima wanga umadana nawo.” Nchifukwa chake amanena kuti, “Akhungu ndi opunduka sadzaloŵa m'Nyumba ya Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lija Davide anati, Ali yense akakantha Ajebusi, aponye m'madzi opuala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Cifukwa cace akuti, Akhungu ndi opuala sangalowe m'nyumbamo.