2 Samuel 5:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adakhala mu mzinda wamalinga uja nautchula dzina lakuti, “Mzinda wa Davide.” Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku malo komwe kale kunali chidikha, kuvuma kwa phiri mpaka m'kati mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anakhala m'linga mula, nalicha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.