2 Samuel 6:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Davide sadafunenso kuti abwere nalo Bokosi la Chautalo kwao ku mzinda wake wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Davide sanafuna kudzitengera likasa la Yehova lidze ku mudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.