2 Samuel 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adamva kuti Chauta wadalitsa banja la Obededomu ndi zinthu zonse zimene anali nazo, chifukwa cha Bokosi lachipangano. Choncho iye adapita kukatenga Bokosi lachipanganolo, kulichotsa m'nyumba ya Obededomu, napita nalo ku mzinda wake, akukondwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumudzi wa Davide, ali ndi chimwemwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obedi-Edomu ndi zace zonse, cifukwa ca likasa la Mulungu. Comweco Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu, nakwera nalo ku mudzi wa Davide, ali ndi cimwemwe.