2 Samuel 6:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Bokosi lachipangano linkaloŵa mu mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina molemekeza Chauta. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pamene likasa la Yehova tinafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikubvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwace.