2 Samuel 6:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nakalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono Davide adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analgka pamalo pace pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.