2 Samuel 6:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli yanyama, ndiponso keke ya mphesa zouma. Tsono anthu onse adachokapo, napita aliyense kunyumba kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israyeli, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa, Ndipo anthu aja onse anabwera yense ku nyumba yace.