2 Samuel 6:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanyamuka, napita pamodzi ndi ankhondo onse amene anali naye kuchokera ku Baala wa ku Yuda kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta. Bokosilo limadziwika ndi dzina la Chauta Wamphamvuzonse, amene amakhala pa akerubi ngati pa mpando waufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nacokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amachula nalo Dzinalo Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.