2 Samuel 6:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Davide adabwerera kuti akadalitse banja lake, Mikala, mwana wa Saulo, adadzamchingamira nati, “Nkutero mfumu ya Aisraele kudzilemekeza kwake lero! Mpaka kuchita kudzivula pamaso pa adzakazi a antchito ake, monga m'mene amachitira munthu wamisala, opanda ndi manyazi omwe!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yace. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Sauli anaturukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israyeli inalemekezeka ndithu, amene anabvula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ace, monga munthu woluluka abvula wopanda manyazi!