2 Samuel 6:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adamuyankha kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Chauta, amene adandisankhula ine kupambana bambo wako, ndiponso kupambana banja lonse la bambo wako. Ndipo adandiika kuti ndikhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta. Choncho ndidzasangalalabe ndi kulemekeza Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anamuyankha Mikala kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Yehova, amene anandisankha ine kupambana abambo ako, kapenanso kupambana banja la abambo ako. Ndipo anandisankha kuti ndikhale wolamulira Aisraeli, anthu a Yehova. Nʼchifukwa chake ndidzasangalalabe pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lace lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israyeli, cifukwa cace ndidzasewera pamaso pa Yehova.