2 Samuel 6:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adatulutsa Bokosi lachipanganolo m'nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri, nalinyamula pa ngolo yatsopano. Tsono Uza ndi Ahiyo, ana a Abinadabu, ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa gareta watsopano, ataliturutsa m'nyumba ya Abinadabu, iri pacitunda, ndipo Uza ndi Ahio ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa gareta watsopanoyo.