2 Samuel 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse ankakondwerera kwambiri kulemekeza Chauta poimba ndi mphamvu zao zonse nyimbo ndi azeze, apangwe, tizing'wenyeng'wenye, maseche ndi ziwaya zamalipenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoyimbira za mitundu mitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi masece, ndi nsanje.