2 Samuel 7:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidakupumitsa kwa adani ako onse. Kuwonjezera pamenepo, Chauta akukuuza kuti, Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse. “ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israyeli; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.