2 Samuel 7:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakhala atate wace, iye nadzakhala mwana wanga; akacita coipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;