2 Samuel 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Davide adaloŵa m'chihema chopembedzeramo Chauta. Adakhala pansi nayamba kupemphera, adati, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nchiyani, kuti Inu mwandifikitsa mpaka pamene ndiliripa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati: “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhalapansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi ciani kuti munandifikitsa pano?