2 Samuel 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Chauta Wamphamvuzonse. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandionetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Kodi umu ndi mmene mumachitira ndi munthu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo icinso cinali pamaso panu cinthu cacing'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikuru irinkudza; ndipo mwatero monga mwa macitidwe a anthu, Yehova Mulungu!