2 Samuel 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndirikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu liri m'kati mwa nsaru zocinga.