2 Samuel 7:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace wamkuru ndi Inu Yehova. Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.