2 Samuel 7:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola ku Ejipito kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamodzi ndi milungu yao, pamene ankafika anthu anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso mtundu uti wa pa dziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso mtundu uti wa pa dziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israyeli, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ace, ndi kuti limveke dzina lace, ndi kukucitirani zinthu zazikuru ndi kucitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwaturutsa ku dziko la Aigupto mwa amitundu ndi milungu yao?