2 Samuel 7:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsopano Inu, Chauta Mulungu, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa. Muchite monga momwe mudaanenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yake, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimuchite monga munalankhula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yace, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimucite monga munalankhula.