2 Samuel 7:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho dzina lanu lidzalemekezedwa mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wolamulira Aisraele.’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wit makamu ndiye Mulungu wa Israyeli, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu.