2 Samuel 7:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Aisraele, mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pemphero limeneli kwa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, munaulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; cifukwa cace mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero gi kwa Inu.