2 Samuel 7:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti mwatero ndinu Ambuye Chauta, choncho banja la mtumiki wanune lidzadalitsidwadi mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake tsono chikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu chikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munachinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace tsono cikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu cikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munacinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.