2 Samuel 7:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine sindidakhalepo m'nyumba chiyambire tsiku limene ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali m'hema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinaturutsa ana a Israyeli ku Aigupto kufikira lero lomwe, kama ndinayenda m'cihema ndi m'nyumba wamba.