2 Samuel 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakucotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israyeli,