2 Samuel 8:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adatuma mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Toi kaŵirikaŵiri. Tsono Yoramuyo adabwera ndi mphatso zopangidwa ndi siliva, golide, ndi mkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Toi anatumiza mwana wace Joramu kwa mfumu Davide, kuti akamlankhule iye, ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezeri ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezeri ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Joramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolidi, ndi zotengera zamkuwa.