2 Samuel 8:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaika zigono za ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu. Mu Edomu monse munali timagulu ta ankhondo, choncho Aedomu onse adasanduka otumikira Davide. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.