2 Samuel 8:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adagonjetsanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pamene Hadadezereyo ankapita kumtunda kwa mtsinje wa Yufurate, kuti akakhazikitsenso ulamuliro wake ku deralo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Davide anakanthanso Hadadezeri, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wace ku cimtsinje ca Firate.