2 Samuel 8:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adagwira ankhondo a Hadadezere. Okwera pa akavalo analipo 1,700, a pansi analipo 20,000. Ndipo adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okakoka magaleta, koma adasungako ena a magaleta 100.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anatenga apakavalo ace cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi maku mi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magareta, koma anasunga a iwo akufikira magareta zana limodzi.