2 Samuel 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adauza mfumu kuti, “Mtumiki wanune ndidzachita zonse potsata zimene inu mbuyanga mfumu mwalamula.” Choncho Mefiboseti ankadya ndi Davide ngati mmodzi mwa ana a mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzacita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.