2 Samuel 9:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Mefibosetiyo adakhala ku Yerusalemu, poti iyeyo ankadya ku nyumba ya mfumu masiku onse. Koma tsono anali wolumala mapazi onse aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ace onse awiri.