2 Samuel 9:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali mtumiki wina wa banja la Saulo, dzina lake Ziba. Ameneyo adamuitana kuti apite kwa Davide. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe Ziba?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene, mtumiki wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Saulo dzina lake Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu amene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?” Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Sauli dzina lace Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu ame.