2 Samuel 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu idamufunsa kuti, “Kodi palibe wina aliyense wa pa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo monga momwe ndidalonjezera kwa Mulungu?” Ziba adayankha kuti, “Padakali mwana wamwamuna wa Yonatani. Iyeyo ngwopunduka miyendo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Sauli kuti ndimuonetsere cifundo ca Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Jonatani wopunduka mapazi ace.