2 Samuel 9:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, adafika kwa Davide, adaŵerama pamaso pake, napereka ulemu. Tsono Davide adati, “Mefiboseti!” Iyeyo adayankha kuti, “Ndabwera ine mtumiki wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yace pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.