2 Samuel 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adamuuza kuti, “Usaope. Ndifuna kukuchitira chifundo chifukwa cha Yonatani bambo wako, ndipo ndidzakubwezera dera lonse la Saulo mbuyako. Udzadya nane pamodzi masiku onse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakucitira kukoma mtima cifukwa ca Jonatani atate wako; ndi minda yonse ya Sauli ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa cikhalire.