2 Thessalonians 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse chomkomera chonse, ndi ntchito ya chikhulupiriro mumphamvu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse comkomera conse, ndi nchito ya cikhulupiriro mumphamvu;