2 Thessalonians 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu, abale, monga kuyenera; pakuti cikhulupiriro canu cikula cikulire, ndipo cicurukira cikondanoca inu nonse, yense pa mnzace;