2 Thessalonians 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma ciyambe cifike cipatukoco, nabvumbulutsike munthu wosayeruzika, mwana wa cionongeko,