2 Thessalonians 2:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zochedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhalapansi ku Kacisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.