2 Thessalonians 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale tsopano lomwe lino uchimo wayamba kugwira ntchito mobisika. Koma zoyenera kuchitikazo sizidzachitika mpaka amene akuletsa uchimowo tsopano atayamba wachotsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti cinsinsi ca kusayeruzika cayambadi kucita; cokhaci pali womletsa tsopano, kufikira akamcotsa pakati.