2 Thessalonians 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikunena zimenezi popeza kuti tikumva kuti pali ena pakati panu amene ali ndi khalidwe laulesi. Anthu ameneŵa sagwira ntchito konse, koma amangoloŵera pa za anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwakedwake, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwacedwace, osagwira nchito konse, kama ali ocita mwina ndi mwina.