2 Timothy 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye achitire chifundo banja la Onesifore, chifukwa iye ankandisangulutsa kaŵirikaŵiri. Sankachita nane manyazi, ngakhale ndinali womangidwa ndi unyolo:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachita manyazi ndi unyolo wanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu achitire chifundo banja lonse la Onesiforo chifukwa ankandisangalatsa kawirikawiri ndipo sankachita nane manyazi ngakhale ndinali womangidwa ndi maunyolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye acitire banja la Onesiforo cifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawiri kawiri, ndipo sanacita manyazi ndi unyolo wanga;