2 Timothy 1:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Mulungu pa tsiku la chiweruzo. Ukudziŵa bwino ndi iwe wemwe kuti adandithandiza kwambiri ku Efeso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
(Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Ambuye pa tsiku lijalo! Ukudziwa bwino momwe iye anandithandizira mʼnjira zosiyanasiyana ku Efeso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
(Ambuye ampatse iye apeze cifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.