2 Timothy 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pokumbukila cikhulupiriro cosanyenga ciri mwa iwe, cimene cinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunike, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.