2 Timothy 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m'ndende chifukwa cha iye, koma umve nao zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu za Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero usacite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wace; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;