2 Timothy 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uziŵakumbutsa zimenezi anthu, ndipo uŵachenjeze kolimba pamaso pa Mulungu kuti asamakangana pa za mau. Kutero kulibe phindu, koma kumangotayikitsa anthu amene akumva kukanganako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uwakumbutse izi, ndi kuwacitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asacite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva.