2 Timothy 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chipatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala cotengera ca kuulemu, copatulidwa, coyenera kucita naco Mbuye, cokonzera nchito yonse yabwino.