2 Timothy 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndarama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,